Jeremias 23
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · Toque num versículo para ver as referências cruzadas.
Nthambi Yolungama
1“Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. 2Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. 3“Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. 4Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
5Yehova akuti, “Masiku akubwera,
pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.
Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
6Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka
ndipo Israeli adzakhala pamtendere.
Dzina limene adzamutcha ndi ili:
Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
7Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ 8koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
Aneneri Onyenga
9Kunena za aneneri awa:
Mtima wanga wasweka;
mʼnkhongono mwati zii.
Ndakhala ngati munthu woledzera,
ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,
chifukwa cha Yehova
ndi mawu ake opatulika.
10Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;
lili pansi pa matemberero.
Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.
Aneneri akuchita zoyipa
ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11“Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.
Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”
12“Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;
adzawapirikitsira ku mdima
ndipo adzagwera kumeneko.
Adzaona zosaona
mʼnthawi ya chilango chawo,”
13“Pakati pa aneneri a ku Samariya
ndinaona chonyansa ichi:
Ankanenera mʼdzina la Baala
ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
14Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu
ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:
amachita chigololo, amanena bodza
ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.
Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.
Kwa Ine anthu onsewa
ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
15Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa
ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,
chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse
ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
16Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;
zomwe aloserazo nʼzachabechabe.
Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,
osati zochokera kwa Yehova.
17Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,
‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’
Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,
‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
18Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?
Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?
Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
19Taonani ukali wa Yehova
uli ngati chimphepo chamkuntho,
inde ngati namondwe.
Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
20Mkwiyo wa Yehova sudzaleka
mpaka atachita zonse zimene
anatsimikiza mu mtima mwake.
Mudzazizindikira bwino zimenezi
masiku akubwerawa.”
21Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,
komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;
Ine sindinawayankhule,
komabe iwo ananenera.
22Iwo akanakhala pa msonkhano wanga
ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.
Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa
kuti aleke machimo awo.”
23Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
ndiye sindine Mulungu?
24Kodi wina angathe kubisala
Ine osamuona?”
“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
25“Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ 26Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. 27Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. 28Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? 29Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
30Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” 31Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” 32Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza
33Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ 34Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. 35Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ 36Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. 37Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ 38Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, 39ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. 40Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”

Você sabia?
Pastores, o Renovo Justo e a Verdadeira Profecia
- No mundo antigo, os governantes eram frequentemente descritos como pastores. Jeremias contrasta os líderes corruptos de Judá, que dispersaram seu povo, com a promessa de um Renovo justo da linhagem de Davi, que reinaria com sabedoria, executaria a justiça e reuniria o rebanho disperso.Fontes: o próprio texto bíblico
- O capítulo contrasta a capital do norte, Samaria, cujos profetas invocavam a divindade fenícia Baal, com os profetas de Jerusalém. Jeremias retrata as falhas morais e as falsas promessas de paz em Jerusalém como tão graves quanto a proverbial maldade de Sodoma e Gomorra.Fontes: o próprio texto bíblico
- Jeremias emprega imagens vívidas para distinguir a genuína revelação divina dos sonhos inventados. A autêntica palavra de Deus é comparada ao trigo nutritivo, ao fogo consumidor e a um martelo que despedaça a rocha, enquanto as falsas profecias são rejeitadas como simples palha.Fontes: o próprio texto bíblico
Notas escritas com auxílio de IA a partir de fontes abertas (Theographic Bible Metadata, CC BY-SA 4.0; Easton’s Bible Dictionary, domínio público) e revisadas antes de publicar.
Lugares deste capítulo
- Egypt · 30.129, 31.308 · versículo 7
- Samaria · 32.276, 35.195 · versículo 13
- Jerusalem · 31.777, 35.234 · versículos 14, 15, 16
Só aparecem lugares com identificação de alta confiança (90% ou mais segundo as fontes acadêmicas reunidas pelo OpenBible). Mapa da época: DARE (Digital Atlas of the Roman Empire), CC BY 4.0; mapa atual: © colaboradores do OpenStreetMap; lugares: OpenBible.info (CC BY 4.0).
Créditos e licença desta tradução
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero The Holy Bible in the Chichewa language of Malawi: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Language: Chichewa Contributor: Biblica, Inc. Ntchito ino imapezeka pansi pa Creative Commons Attribution –ShareAlike 4.0 Chilolezo cha Ponseponse (CC BY-SA). Mukafuna kuona chilolezo chimenechi, pitani pa http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0 kapena lembani kalata ku Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA. Biblica® ndicho chizindikiro choikidwa ndi Biblica ndipo kuti mugwiritse ntchito Biblica® pafunika chilolezo cholembedwa ndi Biblica, Inc. mwini wake. Pansi pa malamulo a chilolezo cha CC BY-SA, mukhoza kukopa ndi kugawira ena ntchitoyi, mosaisintha pokhapokha ngati mukusunga chizindikiro cha Biblica® mosamala ndi mosachisintha. Mukafuna kusintha ntchitoyi kapena kuitanthauzira m’njira inayake, muyenera kuchotsa chizindikiro ichi cha Biblica®. Mukasintha, onetsani bwinobwino zimene mwasinthazo ndipo dziwitsani kuti: “Ntchito yonse ya Biblica, Inc. imene mwatengapo kagawo chabe ikupezeka mwaulere pa www.biblica.com ndi pa open.bible.” Chidziwitso cha umwini chiyenera kuoneka pa tsamba lonena za Mutu wa Nchitoyi kapena pa tsamba lapadera lonena za umwini wa ntchitoyi motere: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m Ntchito mwaichitayo ichitike potsatira malamulo a chilolezo chija (CC BY-SA). Mukafuna kudziwitsa Biblica, Inc. zokhudza matanthauzidwe anu a ntchitoyi, chonde tipezeni pa https://open.bible/contact-us. This work is made available under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4.0 International License (CC BY-SA). To view a copy of this license, visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0 or send a letter to Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA. Biblica® is a trademark registered by Biblica, Inc., and use of the Biblica® trademark requires the written permission of Biblica, Inc. Under the terms of the CC BY-SA license, you may copy and redistribute this unmodified work as long as you keep the Biblica® trademark intact. If you modify a copy or translate this work, thereby creating a derivative work, you must remove the Biblica® trademark. On the derivative work, you must indicate what changes you have made and attribute the work as follows: “The original work by Biblica, Inc. is available for free at www.biblica.com and open.bible.” Notice of copyright must appear on the title or copyright page of the work as follows: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m You must also make your derivative work available under the same license (CC BY-SA). If you would like to notify Biblica, Inc. regarding your translation of this work, please contact us at https://open.bible/contact-us. This translation is made available to you under the terms of the Creative Commons Attribution Share-Alike license 4.0. You have permission to share and redistribute this Bible translation in any format and to make reasonable revisions and adaptations of this translation, provided that: You include the above copyright and source information. If you make any changes to the text, you must indicate that you did so in a way that makes it clear that the original licensor is not necessarily endorsing your changes. If you redistribute this text, you must distribute your contributions under the same license as the original. Pictures included with Scriptures and other documents on this site are licensed just for use with those Scriptures and documents. For other uses, please contact the respective copyright owners. Note that in addition to the rules above, revising and adapting God's Word involves a great responsibility to be true to God's Word. See Revelation 22:18-19. 2025-05-20
Fonte: http://ebible.org/nya/ · eBible.org