Nations Bible

1 Crônicas 17

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · Toque num versículo para ver as referências cruzadas.

Lonjezo la Mulungu kwa Davide

1Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”

2Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.”

3Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati,

4“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’ 5Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena. 6Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”

7Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. 8Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 9Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja; 10monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse.

“ ‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako. 11Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 12Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 13Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo. 14Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’ ”

15Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.

Pemphero la Davide

16Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati,

“Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa? 17Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.”

18“Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu. 19Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse.

20“Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu. 21Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 22Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.

23“Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera, 24kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.

25“Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 26Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 27Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”

Ilustração artística — interpretação, não registro histórico.

Você sabia?

A Promessa de Deus a Davi

  • Ao considerar que morava em um palácio de cedro enquanto a arca da aliança permanecia sob uma tenda, Davi planejou construir um templo para Deus. Em resposta, Deus prometeu que, em vez de Davi construir uma casa para Ele, Deus estabeleceria uma dinastia real duradoura para Davi.Fontes: o próprio texto bíblico
  • Natã foi um profeta influente durante os reinados de Davi e Salomão, surgindo aqui para transmitir a aliança de Deus acerca da futura dinastia e do templo. Registros bíblicos observam que Natã também participou da coroação de Salomão e escreveu relatos históricos dos reinados de ambos os monarcas.Fontes: Nathan · o próprio texto bíblico
  • Na mensagem divina transmitida por Natã, o Senhor lembrou que tirou Davi do pastoreio de ovelhas para liderar Israel. Essa origem humilde como jovem pastor nas colinas de Judá destacou a notável elevação de sua família ao governo real.Fontes: David · o próprio texto bíblico

Notas escritas com auxílio de IA a partir de fontes abertas (Theographic Bible Metadata, CC BY-SA 4.0; Easton’s Bible Dictionary, domínio público) e revisadas antes de publicar.

Lugares deste capítulo

  • Egypt · 30.129, 31.308 · versículos 5, 21

Só aparecem lugares com identificação de alta confiança (90% ou mais segundo as fontes acadêmicas reunidas pelo OpenBible). Mapa da época: DARE (Digital Atlas of the Roman Empire), CC BY 4.0; mapa atual: © colaboradores do OpenStreetMap; lugares: OpenBible.info (CC BY 4.0).

Créditos e licença desta tradução
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
The Holy Bible in the Chichewa language of Malawi: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc.
Language: Chichewa
Contributor: Biblica, Inc.
Ntchito ino imapezeka pansi pa Creative Commons Attribution –ShareAlike 4.0 Chilolezo cha Ponseponse (CC BY-SA). Mukafuna kuona chilolezo chimenechi, pitani pa http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 kapena lembani kalata ku Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® ndicho chizindikiro choikidwa ndi Biblica ndipo kuti mugwiritse ntchito Biblica® pafunika chilolezo cholembedwa ndi Biblica, Inc. mwini wake. Pansi pa malamulo a chilolezo cha CC BY-SA, mukhoza kukopa ndi kugawira ena ntchitoyi, mosaisintha pokhapokha ngati mukusunga chizindikiro cha Biblica® mosamala ndi mosachisintha. Mukafuna kusintha ntchitoyi kapena kuitanthauzira m’njira inayake, muyenera kuchotsa chizindikiro ichi cha Biblica®. Mukasintha, onetsani bwinobwino zimene mwasinthazo ndipo dziwitsani kuti: “Ntchito yonse ya Biblica, Inc. imene mwatengapo kagawo chabe ikupezeka mwaulere pa www.biblica.com ndi pa open.bible.”
Chidziwitso cha umwini chiyenera kuoneka pa tsamba lonena za Mutu wa Nchitoyi kapena pa tsamba lapadera lonena za umwini wa ntchitoyi motere:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m Ntchito mwaichitayo ichitike potsatira malamulo a chilolezo chija (CC BY-SA).
Mukafuna kudziwitsa Biblica, Inc. zokhudza matanthauzidwe anu a ntchitoyi, chonde tipezeni pa https://open.bible/contact-us.
This work is made available under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4‪.0 International License (CC BY-SA). To view a copy of this license, visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 or send a letter to Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® is a trademark registered by Biblica, Inc., and use of the Biblica® trademark requires the written permission of Biblica, Inc. Under the terms of the CC BY-SA license, you may copy and redistribute this unmodified work as long as you keep the Biblica® trademark intact. If you modify a copy or translate this work, thereby creating a derivative work, you must remove the Biblica® trademark. On the derivative work, you must indicate what changes you have made and attribute the work as follows: “The original work by Biblica, Inc. is available for free at www.biblica.com and open.bible.”
Notice of copyright must appear on the title or copyright page of the work as follows:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m You must also make your derivative work available under the same license (CC BY-SA).
‪If you would like to notify Biblica, Inc. regarding your translation of this work, please contact us at https://open.bible/contact-us.
This translation is made available to you under the terms of the
Creative Commons Attribution Share-Alike license 4.0.
You have permission to share and redistribute this Bible translation in any format and to make reasonable revisions and adaptations of this translation, provided that:
You include the above copyright and source information.
If you make any changes to the text, you must indicate that you did so in a way that makes it clear that the original licensor is not necessarily endorsing your changes.
If you redistribute this text, you must distribute your contributions under the same license as the original.
Pictures included with Scriptures and other documents on this site are licensed just for use with those Scriptures and documents.
For other uses, please contact the respective copyright owners.
Note that in addition to the rules above, revising and adapting God's Word involves a great responsibility to be true to God's Word. See Revelation 22:18-19.
2025-05-20

Fonte: http://ebible.org/nya/ · eBible.org

Fale com a gente

Conte de onde você lê, como a Bíblia tem te ajudado ou o que podemos melhorar. Lemos todas as mensagens.