Nations Bible

Jeremías 17

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · Toca un versículo para ver sus referencias cruzadas.

1“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,

lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.

Uchimowo walembedwa pa mitima yawo

ndiponso pa nyanga za maguwa awo.

2Ngakhale ana awo amakumbukira

maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,

pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,

pa mapiri aatali mʼdzikomo.

3Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense

ndidzazipereka kwa ofunkha

kuti zikhale dipo lawo

chifukwa cha machimo

ochitika mʼdziko lonse.

4Mudzataya dziko limene ndinakupatsani

kuti likhale cholowa chanu.

Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu

mʼdziko limene inu simukulidziwa,

chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,

ndipo udzayaka mpaka muyaya.”

5Yehova akuti,

“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,

amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize

pamene mtima wake wafulatira Yehova.

6Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;

iye sadzapeza zabwino.

Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,

mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.

7“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,

amene amatsamira pa Iye.

8Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi

umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.

Mtengowo suopa pamene kukutentha;

masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.

Suchita mantha pa chaka cha chilala

ndipo sulephera kubereka chipatso.”

9Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse

ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.

Ndani angathe kuwumvetsa?

10“Ine Yehova ndimafufuza mtima

ndi kuyesa maganizo,

ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake

ndiponso moyenera ntchito zake.”

11Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo

ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.

Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,

ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.

12Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero

wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.

13Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,

onse amene amakusiyani adzachita manyazi.

Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi

chifukwa anakana Yehova,

kasupe wa madzi amoyo.

14Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;

pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,

chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.

15Anthu akumandinena kuti,

“Mawu a Yehova ali kuti?

Zichitiketu lero kuti tizione!”

16Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.

Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.

Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.

17Musandichititse mantha;

ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.

18Ondizunza anga achite manyazi,

koma musandichititse manyazi;

iwo achite mantha kwambiri,

koma ine mundichotsere manthawo.

Tsiku la mavuto liwafikire;

ndipo muwawononge kotheratu.

Kusunga Tsiku la Sabata

19Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. 20Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ 21Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. 22Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. 23Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. 24Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. 25Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. 26Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. 27Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”

Ilustración artística: una interpretación, no un registro histórico.

¿Sabías que…?

La confianza, el corazón y el día de reposo

  • El estilo de hierro y la punta de diamante eran herramientas antiguas utilizadas para grabar inscripciones profundas y permanentes en piedra o metal. Jeremías emplea esta imagen para resaltar que la idolatría de Judá no era superficial, sino que estaba profundamente grabada en sus corazones y en los cuernos de sus altares.Fuentes: el propio texto bíblico
  • Jeremías contrasta un arbusto solitario en el desierto árido y salitroso con un árbol frondoso plantado junto a una corriente de agua. Un árbol cuyas raíces alcanzan el agua se mantiene verde y produce fruto incluso en años de sequía, representando a quienes confían en Dios en lugar de las fuerzas humanas.Fuentes: el propio texto bíblico
  • Jeremías recibió la instrucción de proclamar el mensaje divino en las puertas de Jerusalén, prohibiendo el traslado de cargas en el día de reposo. Guardar este día aseguraba la continuidad de los reyes en el trono de David y la llegada de adoradores de la tierra de Benjamín, de Judá y del Neguev.Fuentes: el propio texto bíblico · David · Benjamin (patriarch) · Jerusalem

Notas escritas con ayuda de IA a partir de fuentes abiertas (Theographic Bible Metadata, CC BY-SA 4.0; Easton’s Bible Dictionary, dominio público) y revisadas antes de publicarse.

Lugares de este capítulo

  • Arabah · 30.417, 35.151 · versículo 6
  • Jerusalem · 31.777, 35.234 · versículos 19, 20, 21, 25, 26, 27
  • People’s Gate · Hoy: in Jerusalem · 31.777, 35.234 · versículo 19
  • Negeb · 31.245, 34.841 · versículo 26
  • Shephelah · 31.692, 34.875 · versículo 26

Solo aparecen lugares identificados con alta confianza (90 % o más según las fuentes académicas reunidas por OpenBible). Mapa de la época: DARE (Digital Atlas of the Roman Empire), CC BY 4.0; mapa actual: © colaboradores de OpenStreetMap; lugares: OpenBible.info (CC BY 4.0).

Créditos y licencia de esta traducción
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
The Holy Bible in the Chichewa language of Malawi: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc.
Language: Chichewa
Contributor: Biblica, Inc.
Ntchito ino imapezeka pansi pa Creative Commons Attribution –ShareAlike 4.0 Chilolezo cha Ponseponse (CC BY-SA). Mukafuna kuona chilolezo chimenechi, pitani pa http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 kapena lembani kalata ku Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® ndicho chizindikiro choikidwa ndi Biblica ndipo kuti mugwiritse ntchito Biblica® pafunika chilolezo cholembedwa ndi Biblica, Inc. mwini wake. Pansi pa malamulo a chilolezo cha CC BY-SA, mukhoza kukopa ndi kugawira ena ntchitoyi, mosaisintha pokhapokha ngati mukusunga chizindikiro cha Biblica® mosamala ndi mosachisintha. Mukafuna kusintha ntchitoyi kapena kuitanthauzira m’njira inayake, muyenera kuchotsa chizindikiro ichi cha Biblica®. Mukasintha, onetsani bwinobwino zimene mwasinthazo ndipo dziwitsani kuti: “Ntchito yonse ya Biblica, Inc. imene mwatengapo kagawo chabe ikupezeka mwaulere pa www.biblica.com ndi pa open.bible.”
Chidziwitso cha umwini chiyenera kuoneka pa tsamba lonena za Mutu wa Nchitoyi kapena pa tsamba lapadera lonena za umwini wa ntchitoyi motere:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m Ntchito mwaichitayo ichitike potsatira malamulo a chilolezo chija (CC BY-SA).
Mukafuna kudziwitsa Biblica, Inc. zokhudza matanthauzidwe anu a ntchitoyi, chonde tipezeni pa https://open.bible/contact-us.
This work is made available under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4‪.0 International License (CC BY-SA). To view a copy of this license, visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 or send a letter to Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® is a trademark registered by Biblica, Inc., and use of the Biblica® trademark requires the written permission of Biblica, Inc. Under the terms of the CC BY-SA license, you may copy and redistribute this unmodified work as long as you keep the Biblica® trademark intact. If you modify a copy or translate this work, thereby creating a derivative work, you must remove the Biblica® trademark. On the derivative work, you must indicate what changes you have made and attribute the work as follows: “The original work by Biblica, Inc. is available for free at www.biblica.com and open.bible.”
Notice of copyright must appear on the title or copyright page of the work as follows:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m You must also make your derivative work available under the same license (CC BY-SA).
‪If you would like to notify Biblica, Inc. regarding your translation of this work, please contact us at https://open.bible/contact-us.
This translation is made available to you under the terms of the
Creative Commons Attribution Share-Alike license 4.0.
You have permission to share and redistribute this Bible translation in any format and to make reasonable revisions and adaptations of this translation, provided that:
You include the above copyright and source information.
If you make any changes to the text, you must indicate that you did so in a way that makes it clear that the original licensor is not necessarily endorsing your changes.
If you redistribute this text, you must distribute your contributions under the same license as the original.
Pictures included with Scriptures and other documents on this site are licensed just for use with those Scriptures and documents.
For other uses, please contact the respective copyright owners.
Note that in addition to the rules above, revising and adapting God's Word involves a great responsibility to be true to God's Word. See Revelation 22:18-19.
2025-05-20

Fuente: http://ebible.org/nya/ · eBible.org

Habla con nosotros

Cuéntanos desde dónde lees, cómo te ha ayudado la Biblia o qué podemos mejorar. Leemos todos los mensajes.