Nations Bible

Mark 11

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · Tap a verse to see its cross-references.

Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero

1Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake 2nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. 3Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’ ”

4Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula, 5anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?” 6Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite. 7Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo. 8Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda. 9Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti,

“Hosana!

“Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”

10“Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!”

“Hosana Mmwambamwamba!”

11Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.

Yesu Atemberera Mkuyu

12Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. 13Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.

Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

15Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, 16ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu. 17Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”

18Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.

19Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.

Mkuyu Wofota

20Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. 21Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”

22Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. 24Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu. 25Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.” 26(Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

27Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. 28Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”

29Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi. 30Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”

31Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).

33Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”

Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”

Did you know?

Entering Jerusalem

  • This chapter opens as Jesus and his disciples approach Jerusalem and come to Bethphage and Bethany at the Mount of Olives. Bethany was a village on the south-eastern slope, about two miles east of Jerusalem on the road to Jericho, and its name came from the number of palm trees that grew there; Bethphage, very close by, was the limit of a Sabbath day’s journey from the city, 2,000 cubits. The Mount of Olives is named for the olive trees clothing its slopes: a ridge east of Jerusalem, separated from it by the Kidron valley.Sources: the Bible text itself · Bethany · Bethphage · Mount of Olives
  • The name Bethphage means “house of the unripe fig.” The next day, after they had left Bethany, Jesus was hungry and went to a fig tree in leaf, but found nothing on it except leaves, since it was not the season for figs; he said that no one would ever eat of its fruit again. The next morning they saw the tree withered from the roots, and Peter pointed it out.Sources: the Bible text itself · Bethphage
  • Jesus sat on a colt while many in the crowd spread cloaks on the road and others spread branches cut from the fields. Those ahead and those who followed shouted, “Blessed is the coming kingdom of our father David!” David, whose name means “beloved,” was the eighth and youngest son of Jesse, a citizen of Bethlehem. The Mount of Olives is first mentioned in connection with David’s flight from Jerusalem during Absalom’s rebellion.Sources: the Bible text itself · David · Mount of Olives

Notes written with AI assistance from open sources (Theographic Bible Metadata, CC BY-SA 4.0; Easton’s Bible Dictionary, public domain) and reviewed before publishing.

Places in this chapter

  • Jerusalem · 31.777, 35.234 · verses 1, 11, 15, 27
  • Mount of Olives · 31.778, 35.246 · verse 1

Only places identified with high confidence are shown (90% or more according to the scholarly sources compiled by OpenBible). Period map: DARE (Digital Atlas of the Roman Empire), CC BY 4.0; modern map: © OpenStreetMap contributors; places: OpenBible.info (CC BY 4.0).

Credits and license for this translation
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
The Holy Bible in the Chichewa language of Malawi: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc.
Language: Chichewa
Contributor: Biblica, Inc.
Ntchito ino imapezeka pansi pa Creative Commons Attribution –ShareAlike 4.0 Chilolezo cha Ponseponse (CC BY-SA). Mukafuna kuona chilolezo chimenechi, pitani pa http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 kapena lembani kalata ku Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® ndicho chizindikiro choikidwa ndi Biblica ndipo kuti mugwiritse ntchito Biblica® pafunika chilolezo cholembedwa ndi Biblica, Inc. mwini wake. Pansi pa malamulo a chilolezo cha CC BY-SA, mukhoza kukopa ndi kugawira ena ntchitoyi, mosaisintha pokhapokha ngati mukusunga chizindikiro cha Biblica® mosamala ndi mosachisintha. Mukafuna kusintha ntchitoyi kapena kuitanthauzira m’njira inayake, muyenera kuchotsa chizindikiro ichi cha Biblica®. Mukasintha, onetsani bwinobwino zimene mwasinthazo ndipo dziwitsani kuti: “Ntchito yonse ya Biblica, Inc. imene mwatengapo kagawo chabe ikupezeka mwaulere pa www.biblica.com ndi pa open.bible.”
Chidziwitso cha umwini chiyenera kuoneka pa tsamba lonena za Mutu wa Nchitoyi kapena pa tsamba lapadera lonena za umwini wa ntchitoyi motere:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m Ntchito mwaichitayo ichitike potsatira malamulo a chilolezo chija (CC BY-SA).
Mukafuna kudziwitsa Biblica, Inc. zokhudza matanthauzidwe anu a ntchitoyi, chonde tipezeni pa https://open.bible/contact-us.
This work is made available under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4‪.0 International License (CC BY-SA). To view a copy of this license, visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4‪.0 or send a letter to Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA.
Biblica® is a trademark registered by Biblica, Inc., and use of the Biblica® trademark requires the written permission of Biblica, Inc. Under the terms of the CC BY-SA license, you may copy and redistribute this unmodified work as long as you keep the Biblica® trademark intact. If you modify a copy or translate this work, thereby creating a derivative work, you must remove the Biblica® trademark. On the derivative work, you must indicate what changes you have made and attribute the work as follows: “The original work by Biblica, Inc. is available for free at www.biblica.com and open.bible.”
Notice of copyright must appear on the title or copyright page of the work as follows:
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™
Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.
Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™
Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.
“Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo.
“Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m You must also make your derivative work available under the same license (CC BY-SA).
‪If you would like to notify Biblica, Inc. regarding your translation of this work, please contact us at https://open.bible/contact-us.
This translation is made available to you under the terms of the
Creative Commons Attribution Share-Alike license 4.0.
You have permission to share and redistribute this Bible translation in any format and to make reasonable revisions and adaptations of this translation, provided that:
You include the above copyright and source information.
If you make any changes to the text, you must indicate that you did so in a way that makes it clear that the original licensor is not necessarily endorsing your changes.
If you redistribute this text, you must distribute your contributions under the same license as the original.
Pictures included with Scriptures and other documents on this site are licensed just for use with those Scriptures and documents.
For other uses, please contact the respective copyright owners.
Note that in addition to the rules above, revising and adapting God's Word involves a great responsibility to be true to God's Word. See Revelation 22:18-19.
2025-05-20

Source: http://ebible.org/nya/ · eBible.org

Talk to us

Tell us where you read from, how the Bible has helped you, or what we could improve. We read every message.