Ezekiel 29
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · Tap a verse to see its cross-references.
Za Chilango cha Igupto
1Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: 2“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. 3Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
ndinadzipangira ndekha.’
4Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
5Ndidzakutaya ku chipululu,
iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
6Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. 7Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.
8“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. 9Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ 10nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. 11Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. 12Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
13“ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. 14Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. 15Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. 16Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”
Mphotho ya Nebukadinezara
17Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: 18“Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. 19Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. 20Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
21“Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”

Did you know?
Prophecies Against Egypt and Pharaoh
- The expression "from Migdol to Syene" spanned the entire territory of Egypt, from the fortified city of Migdol in the northeast to Syene (modern Aswan) at the southern border adjoining Cush.Sources: Migdol · Syene · Cush · the Bible text itself
- The chapter references the prolonged military effort conducted by Nebuchadnezzar king of Babylon against the city of Tyre, prophesying that his army would seize the wealth of Egypt as payment for their labor.Sources: Nebuchadnezzar · the Bible text itself
Notes written with AI assistance from open sources (Theographic Bible Metadata, CC BY-SA 4.0; Easton’s Bible Dictionary, public domain) and reviewed before publishing.
Places in this chapter
- Egypt · 30.129, 31.308 · verses 2, 3, 6, 8, 9, 10, 12, 13, 14, 15, 16, 19, 20
- Nile · Today: Nile River · 31.465, 30.367 · verses 3, 4, 5, 9, 10
- Cush · Today: Cush 1 · 16.935, 33.751 · verse 10
- Syene · Today: Aswan · 24.089, 32.900 · verse 10
- Pathros · Today: Upper Egypt · 24.100, 32.700 · verse 14
- Babylon · 32.543, 44.422 · verses 18, 19
- Tyre · 33.271, 35.196 · verses 18, 20
Only places identified with high confidence are shown (90% or more according to the scholarly sources compiled by OpenBible). Period map: DARE (Digital Atlas of the Roman Empire), CC BY 4.0; modern map: © OpenStreetMap contributors; places: OpenBible.info (CC BY 4.0).
Credits and license for this translation
Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero The Holy Bible in the Chichewa language of Malawi: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero copyright © 2016, 2002 Biblica, Inc. Language: Chichewa Contributor: Biblica, Inc. Ntchito ino imapezeka pansi pa Creative Commons Attribution –ShareAlike 4.0 Chilolezo cha Ponseponse (CC BY-SA). Mukafuna kuona chilolezo chimenechi, pitani pa http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0 kapena lembani kalata ku Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA. Biblica® ndicho chizindikiro choikidwa ndi Biblica ndipo kuti mugwiritse ntchito Biblica® pafunika chilolezo cholembedwa ndi Biblica, Inc. mwini wake. Pansi pa malamulo a chilolezo cha CC BY-SA, mukhoza kukopa ndi kugawira ena ntchitoyi, mosaisintha pokhapokha ngati mukusunga chizindikiro cha Biblica® mosamala ndi mosachisintha. Mukafuna kusintha ntchitoyi kapena kuitanthauzira m’njira inayake, muyenera kuchotsa chizindikiro ichi cha Biblica®. Mukasintha, onetsani bwinobwino zimene mwasinthazo ndipo dziwitsani kuti: “Ntchito yonse ya Biblica, Inc. imene mwatengapo kagawo chabe ikupezeka mwaulere pa www.biblica.com ndi pa open.bible.” Chidziwitso cha umwini chiyenera kuoneka pa tsamba lonena za Mutu wa Nchitoyi kapena pa tsamba lapadera lonena za umwini wa ntchitoyi motere: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m Ntchito mwaichitayo ichitike potsatira malamulo a chilolezo chija (CC BY-SA). Mukafuna kudziwitsa Biblica, Inc. zokhudza matanthauzidwe anu a ntchitoyi, chonde tipezeni pa https://open.bible/contact-us. This work is made available under the Creative Commons Attribution-ShareAlike 4.0 International License (CC BY-SA). To view a copy of this license, visit http://creativecommons.org/licenses/by-sa/4.0 or send a letter to Creative Commons, PO Box 1866, Mountain View, CA 94042, USA. Biblica® is a trademark registered by Biblica, Inc., and use of the Biblica® trademark requires the written permission of Biblica, Inc. Under the terms of the CC BY-SA license, you may copy and redistribute this unmodified work as long as you keep the Biblica® trademark intact. If you modify a copy or translate this work, thereby creating a derivative work, you must remove the Biblica® trademark. On the derivative work, you must indicate what changes you have made and attribute the work as follows: “The original work by Biblica, Inc. is available for free at www.biblica.com and open.bible.” Notice of copyright must appear on the title or copyright page of the work as follows: Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero™ Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc. Biblica® Open Godʼs Word in Contemporary Chichewa™ Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc. “Biblica” ndilo dzina lodziwika la ntchitoyi ku United States limene linalembetsedwa ndi Biblica mwini. Limagwiritsidwa ntchito ndi chilolezo. “Biblica” is a trademark registered in the United States Patent and Trademark Office by Biblica, Inc. Used with permission.\m You must also make your derivative work available under the same license (CC BY-SA). If you would like to notify Biblica, Inc. regarding your translation of this work, please contact us at https://open.bible/contact-us. This translation is made available to you under the terms of the Creative Commons Attribution Share-Alike license 4.0. You have permission to share and redistribute this Bible translation in any format and to make reasonable revisions and adaptations of this translation, provided that: You include the above copyright and source information. If you make any changes to the text, you must indicate that you did so in a way that makes it clear that the original licensor is not necessarily endorsing your changes. If you redistribute this text, you must distribute your contributions under the same license as the original. Pictures included with Scriptures and other documents on this site are licensed just for use with those Scriptures and documents. For other uses, please contact the respective copyright owners. Note that in addition to the rules above, revising and adapting God's Word involves a great responsibility to be true to God's Word. See Revelation 22:18-19. 2025-05-20
Source: http://ebible.org/nya/ · eBible.org